Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Dr Chakwera adzapambananso chaka chamawa – Mussa

Yemwe anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP m’chigawo chapakati ndipo tsopano analowa Malawi Congress (MCP) a Uladi Mussa, apempha anthu m’dziko muno kuti akhale pambuyo pa Prezidenti Dr Lazarus Chakwera komanso chipani cha MCP, omwe akangalika kutukula dziko lino.

A Mussa amalankhula izi pa msonkhano omwe nduna yazam’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, achititsa pa sukulu ya Mpatsa mdera la pakati m’boma la Nsanje.

Iwo ati Dr Chakwera adzapambananso chaka cha mawa kamba ka ntchito zachitukuko zomwe zikuchitika mdziko muno.

 

Related posts

Tikuyembekeza kuti IMF ikhutitsidwa ndi kayendetsedwe ka chuma — Chithyola Banda

Romeo Umali

Aliyense atenge gawo posamala misika — Khonsolo ya Lilongwe

Romeo Umali

Ndende zisintha – Boma

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.