Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Amagulitsa mwana wake wazaka zitatu

Apolisi ku Nkhunga m’boma la Nkhotakota amanga amuna awiri powaganizira kuti amatsatsa malonda a mwana wazaka zitatu.

Mneneri wapolisi ya Nkhunga, Andrew Kamanga, wati amunawo ndi Pilirani Thumba wazaka  38 yemwe ndi bambo wamwanayo komanso Yohane Watch wazaka 48.

A Kamanga ati apolisiwo anatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti pali abambo ena omwe akugona pamalo ogona alendo pasitolo za pa Dwangwa ndipo akugulitsa mwana.

Apolisiwo atafika pamalopo, anapeza amunawo ndipo atawafunsa anavomera kuti akugulitsa mwanayo.

Related posts

Government hails creative industry growth as COSOMA disburses K1.8 billion in royalties

McDonald Chiwayula

China/Malawi sign MK 50bn judicial complex grant agreement

MBC Online

Let’s work together to contain economic challenges — MCCCI

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.