Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

Serengeti Energy yagulitsa 21 megawatts ku ESCOM

Kampani yopanga magetsi kuchokera kumphamvu ya dzuwa, Serengeti Energy, yati yayamba kugulitsa magetsi okwana 21 megawatts ku kampani ya ESCOM pofuna kuthana ndi vuto lakuzima kwa magetsi.

M’modzi mwa adindo ku Serengeti Energy, a Paul Mhango, ati ndi okondwa kuti ayamba kuthandizira nawo pa ntchito yothana ndi vuto lamagetsi m’dziko muno.

Iwo anati akukonza zokhazikitsanso malo ena komwe ayikenso magetsi a mphamvu ya dzuwa m’boma la Nkhotakota, kumene kuli kampani yawo.

A Mhango ati akuonetsetsa kuti akugwira ntchito limodzi ndi anthu a m’bomali kuphatikizapo kupereka mwayi wa ntchito kwa achinyamata.

Ofalitsankhani wa bomali, a Wongani Mkandawire, ati kubwera kwa kampaniyi kwathandizira kuthana ndi vuto lakuthima kwa magetsi m’bomali kumene kumafika alendo ambiri.

Kuyambira pa 29 July chaka chatha, kampani ya Serengeti Energy ndi imodzi mwa kampani zoyima pazokha zomwe zimapanga magetsi a mphamvu ya dzuwa ndi kugulitsa ku ESCOM.

 

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

FCB commits to supporting business journalists

MBC Online

Petroleum importers provides safe water to Linyangwa Health Centre

Olive Phiri

Asilikali agwira nzika 276 zozembetsedwa zaku Ethiopia

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.