Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Sankhani moyenera zokaphunzira ku university’

Phungu wadera la Kumachenga m’boma la Lilongwe a Ezra Ching’onga adandaula kuti ophunzira ambiri omwe amalemba mayeso a MSCE mdera lake sasankhidwa kupita ku university chifukwa amalephera kusankha moyenera ma programme aku university mogwirizana ndi momwe akhonzera mayeso a MSCE.

“Ophunzira mdera lathu amakhonza mayeso a MSCE koma sapita ku sukulu zaukachenjede. Chitsanzo ena amakhoza  ndi ma points oposa makumi awiri, koma akufuna maphunziro azasayansi  monga engineering, a NCHE angamutenge ?” anadandaula choncho a Ching’onga.

Iwo anati kusankha moyenera kungatheke ndi thandizo la aphunzitsi komanso makolo amene ali ndikuthekera.

Iwo ayankhula izi pamwambo otsanzikana ndi ophunzira a Form 4 apa sukulu ya Njewa Community Day.

Mphunzitsi wamkulu pa sukulupo a Emmanuel Mponda ati ayesetsa kuwunikila achinyamatawo pa zisankho zoyenera.

 

Related posts

‘Mkumano wa Chakwera, achinyamata chikhale chiyambi’

Romeo Umali

M0626 finale this afternoon

Yamikani Simtowe

Chakwera attending memorial service for late Namibian President Hage Geingob

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.