Anthu ochuluka asonkhana ku nyumba ya chisoni ya Sunset Funeral Services ku Kanengo munzinda wa Lilongwe komwe pali chikonzero chonyamula ena mwa matupi a anthu omwe adafa pangozi ya ndege limodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima.
Pali chiyembekezo choti pa mwambowu pakhalanso mwambo wa Misa poremekeza mzimu wa mayi Patricia Shanil Dzimbiri, omwe anaakhalapo mayi wa dziko lino zaka za mmbuyomu.
Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, komanso mayi wa dziko lino, Madam Monica Chakwera, akuyembekezeka kukhala nawo pamwambowu.