Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

UK yathandiza Lake of Stars ndi K169 Miliyoni

Boma la Britain lathandiza chikonzero cha nyimbo la Lake of Stars ndi ndalama zokwana pafupifupi K169 miliyoni ngati mbali imodzi yolimbikitsa ubale pakati pamaiko awiriwa.

Kazembe wadziko la Britain kuno ku Malawi a Fiona Ritchie alengeza izi lero  pomwenso kwangotsala masiku ochepa kuti phwandoli lichitike.

A Ritchie ati thandizoli ndilofuna kusintha chithunzithunzi chomwe chilipo maka chongothandizana panthawi ya zovuta komanso kulimbikitsa ubale wamaikowa komanso kutukula nkhani zamsangulutso.

Phwandoli likubwera patatha zaka zinayi  lisakuchitika.

A Sharmila Elias ndi mkulu yemwe akuyendetsa phwando la Lake of Stars ndipo wayamikira boma la Britain kamba kathandizoli.

Phwando la oimba la Lake of Stars lomwe lichitike kwamasiku atatu m’mboma la Nkhotakota lichitika pokondwekeranso  kuti lakwanitsa zaka makumi awiri tsopano chiyambire kusangalatsa anthu ndi kutukula oyimba mdziko muno powapatsa danga loonetsa luso lawo Ku dziko lonse.

Related posts

Bullets in FDH Semis

Romeo Umali

Old Mutual donates K7 million to support MIAC’s symposium

Romeo Umali

‘Malo nawa koma tionepo chitukuko pasanathe zaka ziwiri’

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.