Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, lero akawonekera ku nyumba ya malamulo ndikukayankha mafunso kuchokera kwa aphungu anyumbayi.
Potsimikiza izi, mneneri wa Boma, a Moses Kunkuyu, wati President Chakwera akawonekera ku nyumbayi pokwaniritsa malonjezo ake woti adzakhala wotumikira anthu a m’dziko muno poyankha mafunso kudzera kwa aphungu awo.
Mtsogoleri wadziko linoyu akakhala ali ku nyumba ya malamulo masana ano kuyambira nthawi ya 2 koloko.
Wolemba: Timothy Kateta
#MBCOnlineServices