Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera wasankha a Jacob Mazalale ngati mlembi mu unduna wa zachuma oona za mapulani achitukuko.
A Mazalale, amene ndi mphunzitsi wazachuma pa sukulu yaukachenjede ya Unima ku Zomba, adzikayang’ana nkhani zokhudza mapulani achitukuko ndi chuma ku undunawu.
Mneneri ku ofesi ya mlembi wa mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna zake, a Robert Kalindiza, atsimikiza za nkhaniyi.
A Kalindiza ati Dr Chakwera asankha a Mazalale ndicholinga chofuna kuwonetsetsa kuti chuma cha dziko lino chipitilire kubwelera mchimake.