Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Ntchito yomanga misewu ikuyenda bwino ku Lilongwe’

Ena mwa anthu amene amagwiritsa ntchito misewu ya mu mnzinda wa Lilongwe ati ndi okondwa ndi mmene ntchito yomanga misewu mu mnzindawu ikuyendera.

Poyankhula ndi MBC, a Biliati Basikolo amene amayendetsa minibus yoyenda ku Area 25 kupita mu tauni ya Lilongwe ati ndi wokondwa kuona momwe roundabout ya Amina yasinthira mu kanthawi kochepa munzindawu.

“Tikamayenda pena kumaona ngati tili kunja kwa dziko lino. Misewu yake ikukhala yapamwamba,” anatelo a Basikolo.

Malinga ndi malipoti, misewu imene ikumangidwa monga wa Mzimba Street, Kanengo-Crossroads ndi Kenyatta Drive ikhoza kutha mwachangu poyerekeza ndi mmene oyendetsa ntchitoyi amaganizira poyamba.

Mseu wa Kanengo-Crossroads akumanga  ndi a kampani ya Shadong Liquao ya mdziko la China ndi thandizo la ndalama zoposa K22 billion.

Msewu wa Mzimba Street akumanga ndi a kampani ya Mota Engil.

Related posts

‘Tileke kugwiritsa ntchito mapepala opyapyala’

Romeo Umali

President Chakwera to attend Sub-Region Catholic Bishops conference

Romeo Umali

Local authorities urged to lead implementation of physical development plans

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.