M’busa wa mpingo wa Synagogue Pentecostal Church Prophet Millward Nyangulu wapereka thandizo la matumba a chimanga 200 komanso ndalama zokwana K6 million ku Home of Hope Ku Mchinji zoti zithandizire kusamala ana omwe amawasunga pa malopa.
Msungichuma wa mpingowu a Violet Phiri wati achita izi pofuna kuyamikira ntchito yomwe mwini wa malowa m’busa John Chipeta akugwira posamalira anawa.
A Phiri ati mpingowu upitiliza kuthandiza malowa ndipo apempha anthu akufuna kwabwino kuti achitepo kanthu ndi kuthandiza malowa.
“A Khristu tikuyenela kuchita chikondi osati kungoyankhula. Gogo Chipeta ndi munthu wankulu ndipo ntchito imeneyi imayenera izigwiridwa ndi achichepere,” atero a Phiri.
Ndipo m’mau ake Gogo Chipeta ati iwo anayamba malowa pozindikira kuti pali ana ambiri a nzeru omwe akukanika kupeza maphunziro kaamba ka umasiye komanso kuchepekedwa. Iwo athokoza Prophet Milward kamba ka thandizoli.
Pakadali pano malo a Home of Hope akusunga ana amasiye oposa 750.
Malinga ndi a Phiri thandizoli lakwana K15 miliyoni.
Olemba: Beatrice Mwape