Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local News Nkhani

Mlandu wa Bushiri wayima kaye!

Bwalo lamilandu la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe layamba laima kaye kumva mulandu omwe boma la South likufuna kuti Banja la a Bushiri lipite mdzikolo kukayankha milandu yomwe anawatsegulira kufikira pa 17 July Chaka chino.

Bwaloli laimitsa mlanduwu chifukwa mkulu oyimira boma komanso yemwe akutsogolera mlanduwu, a Dzikondianthu Malunda, akuti akudwala.

Mmodzi mwa oimira banja la a Bushiri, a Annelene Van De Heever, anati mbali yawo ndiyokonzeka kupitiriza kufunsa mboni yaboma zokhudza mlanduwu.

Bwalo lamilanduli linayamba kumvanso mlanduwu lachitatu sabata ino atauimitsa mu March chaka chino kuti mbali yoimira ozengedwa ikonzekere mokwanira.

 

Related posts

Mlambe Hospital goes solar

Romeo Umali

CHAKWERA ARRIVES IN NEW YORK

MBC Online

State parades three witnesses in Chisale case

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.