Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Madam Chakwera afika ku mwambo okumbukira tsiku la anthu achialubino

Mayi wa pfuko lino Madam Monica Chakwera afika pa bwalo la masewero la m’boma la Rumphi komwe ali nawo pa mwambo okumbukira tsiku la anthu achialubino.

Mwazina, atafika pabwalopa, Madam Chakwera anayendera zionetsero zomwe akonza a mabungwe omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana zothandiza anthuwa.

Nduna yoona za chisamaliro cha anthu a Jean Sendeza komanso nkulu wabungwe la United Nations m’dziko muno a Rabbacca Addah Donto  komanso anthu osiyanasiyana ndi akuluakulu aboma ali nawo pamwambowu.

Patha zaka khumi tsopano kuyambira pomwe dziko la Malawi linayamba kuchita nawo chikondwererochi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Amumanga ku Kamuzu Central chifukwa chakuba mankhwala

Mayeso Chikhadzula

Amulamula akagwire ndende yakalavula gaga chifukwa chopezeka ndi chida choopsa

Davie Umar

Kampani yatsopano ya magetsi adzuwa ikubwera

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.