Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

FDH Bank yathandiza NFRA ndi chimanga

FDH Bank yapeleka chimanga chokwana matani 100 ku bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA).

Mkulu wa zamalonda ku Banki ya FDH, a Levie Nkunika, wati achita izi potsatira pempho la mtsogoleri wa dziko lino loti dziko lino lili pa ngozi yanjala.

M’mawu ake, mkulu wa bungwe la NFRA, a George Macheka, wati ndikofunika kugwiranamanja pa ntchito yothandiza mabanja amene akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.

Malinga ndi NFRA, dziko lino likufunika pafupifupi ma tani 200,000 kuti lithane ndi vuto lanjara.

Related posts

Bande apempha mafumu atsogolere chitukuko

Blessings Kanache

Achinyamata asamalire okalamba — Mayi Mbambande

Romeo Umali

Chakwera walangiza aMalawi kuti asamvere andale abodza

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.