M’modzi mwa abusa amene amatumikira m’dziko la United Kingdom koma kwawo ndi kuno ku Malawi, Chance Munthari, wati aMalawi akuyenera kusiya kuloza zala ena pamavuto amene dziko lino likukumana nawo.
Munthari wati zambiri m’dziko muno zitha kusintha ngati aliyense payekhapayekha angatengepo gawo pakusintha kaganizidwe ndikuyamba kukhulupilika komanso kutenga udindo pazinthu zing’onozing’ono.
“Ngati tikufuna dzikoli lipite patsogolo ndipofunika ife ngati anthu tiyambe kudziunika patokhapatokha pazolakwika zomwe tikupanga.Tisanadzudzule atsogoleli zakatangale tionenso kuti ifeyo zomwe sitikukhonza ndiziti,” iye anatero.
Iye wati akufuna akhazikitse utumiki wake kuno ku Malawi.
M’busa Munthari ali m’dziko muno pomwe akhale ndi usiku wa kulambira lachisanu ku Golden Peacock mu mzinda wa Lilongwe komwe kukakhale oyimba monga Paul Kachala, Chigo Grace, Pastor Moffat Mtegha komanso Theresa Phondo.