Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Apereka njinga zamoto zothandizira ntchito zaumoyo

Bungwe la Malawi Network of People Living with HIV and AIDS (MANET+) lapereka njinga yamoto ku ofesi ya zaumoyo ya Mzimba North yomwe ithandizire pantchito za umoyo m’bomali.

Mkulu wa bungweli, a Lawrence Khonyongwa ati njingayi ndi gawo la ntchito yaikulu yotukula zaumoyo yomwe ikulandira thandizo kuchokera kuthumba la Global Fund.

“Ili ndi gawo la chitatu la ntchito yotchedwa COVID-19 Response Mechanism yomwe cholinga chake ndikuyika dongosolo lokonzekera mavuto ena aliwonse omwe angagwe mwadzidzidzi,” anatero a Khonyongwa.

Iwo anati matenda a COVID 19 anapereka maphunziro osiyanasiyana ndikuti limodzi mwamaphuzirowa ndikukhala okonzeka.

A Khonyongwa anati njingazi azigawanso mmaboma a Likoma, Rumphi komanso Nkhotakota.

 

Olemba Henry Haukeya

Related posts

Jenda Police nets two unlicensed hemp possessors

Romeo Umali

HSAs in Balaka get bicycles to improve healthcare

MBC Online

Chimwendo Banda ayamika Chakwera poyika amayi m’maudindo akuluakulu

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.