Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Dr Usi ati adzipereka pofuna kukweza miyoyo ya a Malawi

Wachiwiri watsopano kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wati adzipereka kwathunthu kuthandiza Prezidenti Dr Lazarus Chakwera potukula dziko lino komanso kukweza aMalawi.

Iwo anena zimenezi ku Nyumba ya Malamulo munzinda wa Lilongwe pamwambo owalumbiritsa kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Iwo alowa mmalo mwa Dr Saulos Klaus Chilima ene anali pa udindowu kufikira imfa yawo pa ngozi ya ndege yomwe inagwa pa 10 June.
Iwo ati ati alandira udindowu ndi nsangala komanso chisoni — chisoni kaamba koti Dr Chilima lero palibepo.

Iwo athokonzanso Dr. Chakwera kaamba kowakhulupilira powapatsa ntchito zosiyanasiyana m’boma monga nduna ndipo pano powasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Iwo apemphanso anthu mdziko muno kuti akhale ogwirizana kuti chitukuko chipitilire kuyenda bwino.

Dr. Usi atinso alimbikitsa ntchito za chipani cha UTM.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Agwidwa ndi mankhwala oopsya ozunguza bongo

Chakwera appoints ministerial committee for VP state funeral

Doreen Sonani

LL Police nabs TikToker for suspected fraud

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.