Anthu ena alipanja pa nyumba ya malamulo pomwe ayika kanema pofuna kupereka mwayi kwa anthuwo oonelera mwambo wolumbilitsa Dr Michael Bizwick Usi kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.
Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, yemwe wasankha a Usi kukhala wachiwiri wawo, ndi mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera alinawo pamwambowu.
Dr Usi awasankha pampandowu potsatira imfa ya malemu Dr Saulos Klaus Chilima pa ngozi ya ndege limodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.