Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Blue Eagles yatsala ndi ma poyinsi atatu kuti ibwerere mu super league

Timu ya Blue Eagles yalimbikitsa mwayi wake obweleranso mu ligi yaikulu ya TNM pomwe yagonjetsa Ekas Freight Wanderers ndi zigoli zinayi kwa zero pabwalo la Airport Development Limited munzinda wa Lilongwe.

Ganizani James, Laurent Banda, Tonic Vivuyi ndi Miccium Mhone ndiomwe anamwetsa dzigolizi zomwe zapangitsa kuti timuyi idzitsogola ndi mapoinsi 12. Eagles ili ndi ma poyinsi 48 itasewera masewero 18 pomwe Villa yomwe ndiyachiwiri ili ndi ma poyinsi 36 itasewera masewero 17.

Izi zikutanthauza kuti  Eagles yomwe siinangonjepo mu ligi ya Chipiku ikungofunika mapoyinsi atatu pamasewero anayi omwe yatsala nawo,  Koma mphuzitsi wa timuyi Eliya Kananji wati anyamata ake satayirira  chifukwa ulendo wobwelera mu Super League sunatheke.

Zotsatira zamasewero ena omwe aseweredwa lero, Armour Battalion yagonjetsa Wimbe United 3 – 0, St Gabriel Zitha yathambitsa Extreme 3 – 0, pomwe Mitundu Baptist yagonja ndizigoli ziwiri  pakhomo ndi timu ya Mbadzi United.

Related posts

CS-EPWP enhances sanitation at CBCCs in Rumphi

Rabson Kondowe

Chiradzulu moves to address ARV default rate

Rabson Kondowe

FDH Bank raises cup stakes

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.