Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Anayi ali m’chitokosi ataba mowa wa K2.3 million

Apolisi m’boma la Mangochi amanga anthu anayi amene akuwaganizira kuti anathyola ndi kuba zakumwa zaukali zandalama pafupifupi K2.3 million pa malo ena ogulitsira mowa otchedwa ‘Pa Soko’.

Ofalitsankhani pa Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, anati mowa wina obedwa wapezeka ndipo mabotolo ena apezeka opanda kanthu.

“Mwini wake wa malowa anatidziwitsa kuti usiku wapa 8 September anatseka malowo cha m’ma 1 koloko m’mawa, koma kunja kutayera anazindikira kuti malowo anathyoledwa ndi anthu aupandu komanso anaba ndalama zokwana K120,000,” a Daudi anatero.

Anthu amene akuwaganizirawa ndi a Bongani Kachingwe, 26, Vincent Makhiringa, 32, Maxwell Shafi, 20 komanso Mkwanda Shahid, 22 ndipo akaonekera kubwalo lamilandu kuti akayankhe mulandu otchola nyumba ndi kuba katundu.

 

Related posts

TNM ipereka mabandulo aulere kwa makasitomala ake popilira kuvuta kwa internet

Romeo Umali

National Bank, CAT for revitalised banana productivity

Romeo Umali

Ministry of Tourism wants innovation in the sector

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.