Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Agwetsa sitolo zomangidwa malo osavomerezeka

A khonsolo yamzinda wa Lilongwe, mogwirizana ndi asilikali achitetezo, agumula ndikusalaza sitolo zimene zinaamangidwa mphepete mwa manda ku dera la Nsungwi ku Area 25 ku Lilongweko.

Malinga ndi anthu amene atitsina khutu, izi zachitika kum’bandakucha walero loweruka.

Asanagwetse pa maoneka chonchi. 
Atagwetsa pa maoneka chonchi.

M’mbuyomu, anthu okhala mderali adakachita zionetsero ku ofesi za khonsolo yamzindawu ndikuopseza kuti achitapo kanthu ngati akuluakulu akhonsoloyi sakagwetsa sitolozi.

Iwo ankadandaula kuti sitolozi zidamangidwa kufupi kwambiri ndi manda.

Kanema: Social media

#MBCOnlineServices

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Manja SDA ikutsekera msonkhano wa Misasa

Simeon Boyce

Local chiefs in Dedza speak highly of NEEF loans

Sothini Ndazi

Bullets open Airtel Top 8 with a victory

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.