Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Tabitha wakankha chikopa mogometsa mu February ku France

Katswiri wampira wamiyendo wadziko lino Tabitha Chawinga walandira mendulo ngati osewera mogometsa m’mwezi wa February 2024 mu ligi yayikulu ya mpira wa miyendo ya amayi m’dziko la France.

Chawinga anayamikira anzake amene amasewera nawo ku timu yake ya Paris Saint-Germain (PSG) Féminines,ponena kuti ndiwo apangitsa kuti apeze mphothoyi.

Msungwanayu akutsogola pa m’ndandanda wa omwetsa zigoli mu ligiyo, atamwetsa zigoli zakwana 13 pa masewero 17.

Aka ndi koyamba kuti katswiriyu alandire menduloyi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Abusa asiye kudalira nkhosa zawo pachuma

Chisomo Break

Sizoona kuti chiphaso (Passport) chikhala ndi masamba ochepa — Immigration

Justin Mkweu

Civil defeated, draw for Wanderers

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.