Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Boma lagawa chimanga ku Zomba

Boma lakhazikitsa ntchito yogawa chimanga kwa mabanja pafupifupi 8000 amene njala inawakhudza munzinda wa Zomba.

Mwambo okhazikitsa ntchitoyi unachitika Lachitatu ku Matawale kwa mfumu yayikulu Mwambo munzindawu.

Mkulu wa khonsolo ya Zomba, Archangel Bakolo, wati thandizolo labwera mu nthawi yake kaamba kakuti anthu 17 mwa anthu 100 aliwonse ndi amene njala idawakhudza.

Kudzera ku DoDMA, boma likhala likupereka chimangacho kwa miyezi isanu kuchokera mwezi uno.

Banja lililonse likulandira thumba lolemera makilogalamu 50.

Related posts

Anthu ena akuonera nawo mwambo panja pa nyumba ya malamulo

Mayeso Chikhadzula

Dr Chakwera calls for faith in nation-building

MBC Online

Silver Strikers are 2025 FDH Bank Champions!

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.