Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

Zinthu zambiri zasintha — Chithyola Banda

 

Nduna yoona zachuma, a Simplex Chithyola Banda, ati zinthu zambiri zasintha ndipo chuma chayamba kubwelera m’chimake.

Iwo amayankhapo pa lipoti la bungwe la Afrobarometer limene kafukufuku wake anachitika chaka chatha koma latulutsidwa mwezi uno.

Lipotili lati panthawi yomwe ankapanga kafukufuku, a Malawi ambiri anawonetsa kusakondwa ndi m’mene chuma chinkayendera panthawiyo.

Koma a Chithyola Banda ati pofika pano, zambiri zasintha.

Iwo ati mwachitsanzo, vuto la mafuta linatha, mitengo yachakudya ikutsika, mayiko ndi mabungwe ayambiranso kuthandiza dziko lino komanso kusowa kwa ndalama zakunja kwachepa.

Ndunayi yawonjezeranso kuti zinthu zipitilira kuchita bwino pansi pa ndondomeko ya zachuma imene aphungu akuyikambirana.

“Ndikuwalimbikitsa kuti adzachitenso kafukufuku wina miyezi itatu ikubwerayi, adzapeza zotsatira zosiyana kamba koti zinthu zikusintha tsopano,” a Chithyola Banda anatero.

 

Related posts

‘Do not lock up a child with disability’

MBC Online

LIMBE POLICE STATION MOVES CLOSER TO PEOPLE

MBC Online

BWALO LA MILANDU LABWEZA GALIMOTO YA UMBONI WABOMA

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.