Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Nankhumwa akhazikitsa chipani

Mtsogoleri wa chipani chatsopano cha People’s Development (PDP), Kondwani Nankhumwa, wati chipanichi chabwera kudzasintha Malawi kukhala dziko lodzidalira pa chakudya, la umodzi ndinso kulimbikira pantchito.

Poyankhula pamsonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre, iwo ati chipanichi chithetsa m’chitidwe okakamira m’maudindo muzipani.

A Nankhumwa atinso a Malawi akufunika chipani chomwe chingamalore anthu kupikisana momasuka.

Wolemba: Blessings Cheleuka

Related posts

Fodya akadali ndi tsogolo lowala – Chithyola Banda

Rabson Kondowe

Ena otsatira UTM atsutsa zotsatira zachisankho

Romeo Umali

Ayamikira Chitukuko cha milatho

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.