Bungwe lina limene likudzitcha kuti Concerned Teachers of Malawi lati ndi lokondwa kaamba kakuti ndondomeko zolembetsera aphunzitsi komanso ndalama yolembetsera yatsika.
Mlembi wa bungweli, a Azeez Losa, ati ili ndiyankho pa pempho lawo limene m’mbuyomu adakapereka ku unduna wa zamaphunziro komanso bungwe la Teachers’ Council of Malawi, limene limayang’anira aphunzitsi m’dziko muno.
A Losa amayankhula izi pa msonkhano wa olembankhani mumnzinda wa Lilongwe, ndipo anatinso ndi okhutira ndi njira yamakono yogwiritsa ntchito lamya za m’manja polipilira ndalama yolembetsera aphunzitsi.
“Chomwe chatsala ndikuti aphunzitsi amene alembedwa ntchito mwa ganyu apatsidwe ntchito yokhazikika poti aphunzitsi tikuchepabe ndipo ana ndi ambiri,” iwo anatero.
Pa 8 April chaka chino, bungweli linalembera kalata bungwe la Teachers Council of Malawi ndipo mu kalata yawo, adapempha kuti adindo awunikire mavuto amene aphunzitsi amakumana nawo polembetsa.
Olemba: Paul Mlowoka ndi Thokozani Jumpha