Omwe akuyendetsa phwando la nyimbo la Burning Spear atsimikiza kuti phwandoli litheka kaamba koti ichi ndi chikonzero chake kuti adzayimbe ku Malawi asanapume kuimba.
Mkulu wa Sound Addicts, a Shadreck Kalukusha pamodzi ndi a Sound System Club & Bon Afrikan Productions, ati zonse zili mchimake ndipo katswiri wa chamba cha Reggae yu abwera ndi gulu lake la anthu 17.
Burning Spear yemwe ali ndi zaka 79 ndipo akuyembekezeka kupuma pamaimbidwe, adzaimba m’dziko muno pabwalo Civo mwezi wa October.
Malawi ndi limodzi mwa maiko asanu ndi limodzi omwe nsalamangweyi iyimbe isanpume.
Izi zikutanthauza kuti aka kakhala koyamba ndikotsiriza kuimba kuno ku Malawi.
Olemba: Emmanuel Chikonso