Ena mwa atsogoleri amipingo m’dziko muno ati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera waonetsa kusakondera kwake posankha anthu atsopano m’ma board a kampani za boma.
Prezidenti Chakwera posachedwapa wasankha anthu atsopano kuti athe kutumikira m’ma board a kampanizi.
Chikalata chomwe bungwe lalikulu lama Sheikh m’dziko muno la Ulama Council latulutsa chati Dr Chakwera waonetseratu poyera kuti boma lake limaganizira kwambiri kuti anthu achipembezo cha chisilamu atha kuthandiza nawo kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.
M’mau ake, mlembi wamkulu wa mpingo wa Livingstonia CCAP Synod, m’busa William Tembo, anati zomwe Prezidenti Chakwera wachita zithandiza kulimbikitsa mgwirizano pakati anthu azipembedzo zosiyanasiyana m’dziko muno.
Pothilirapo ndemanga, m’busa Yolamu Nyirenda wati kampani komanso mabungwe osiyanasiyana m’dziko muno atengerepo phunziro posankha anthu mosaganizira zipembedzo komanso komwe akuchokera.
Mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pa nkhani zachipembedzo, m’busa Brian Kamwendo, wati Prezidenti Chakwera apitiriza kukwaniritsa mfundo zake zonse zomwe anawalonjeza aMalawi.
Olemba: George Banda