Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Asiya zolemba, akufuna ku nyumba ya malamulo

Pamene ntchito yokonzekera chisankho chapa 16 September ikuyandikira, tsopano zadziwika kuti atolankhani odziwika bwino opitilira khumi ndi asanu-15 awonetsa chidwi pa ndale ndipo akonzeka kudzapikisana nawo pa chisankhochi.

Atolankhaniwa adzapikisana nawo pa udindo wa aphungu aku nyumba ya malamulo.

MBC Digital yapeza kuti chiwerengerochi chitha kukwera kaamba koti aliponso atolankhani ena omwe sanabwere poyera nkulengeza chidwi chawo chodzapikisana nawo pachisankhochi.

Ena mwa atolankhani odziwika bwino omwe akupikisana nawo pa chisankhochi koyamba ndi Ali Blessings Idi, Luke Chimwaza, Wisdom Chimgwede, Noel Mkubwi, Robert Kalindiza, Jonah Pamkuku, Frank Jomo ndi Anthony Masamba.

Wisdom Chimgwede, mmodzi mwa atola nkhani amene akupikisana nawo.

Padakali pano bungwe la atolankhani la Media Institute of Southern Africa (MISA) Malawi kudzera mwa wapampando wake Golden Matonga layamikira atolankhaniwa kaamba kolimba mtima kuti adzapikisane nawo pa chisankhochi.

M’mau ake katswiri pa ndale George Chaima wati atolankhani ali ndi zowayenereza kuchita ndale chifukwa choti kudzera mu ntchito yawo amatha kukhala pafupi ndikumva bwino lomwe zinthu zomwe anthu akudutsamo. A Chaima ati atolankhani amacheza ndikudziwa mokwanira zofooka za anthu ena pa ndale.

Golden Matonga, wapampando wa bungwe la MISA Malawi

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission likavomereza atolankhaniwa kupikisana nawo ndiye kuti tsopano ayamba ulendo omwe munadutsa kale atolankhani ena odziwika  monga Malemu Jolly Kalero, Malemu Moses Dossi, Aisha Mambo Adams, Joshua Malango ndi Mike Bango kungotchulapo atolankhani ochepa.

Komano funso nkumati kutchuka komwe anatchuka anthuwa kungawathandize kudzakolola mavoti omwe adzawatengere ku nyumba ya malamulo? Yankho la funsoli lidzapezeka pa 16 September chaka chino.

 

Olemba: George Banda

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FAM sacks Mabedi

Romeo Umali

GEFT ichepetsa mavuto obwera ndi kusintha kwa nyengo — Boma, UNDP

Austin Fukula

PROPHET MILWARD APEREKA THANDIZO LA K15 MILION KWA ANA A MASIYE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.