Bungwe la Islamic Information Bureau munzinda wa Mzuzu lalimbikitsa achinyamata kuti akhale ndi mtima okonda kuwerenga mabuku ndi cholinga chakuti ziwathandize kuchita bwino pa maphunziro awo.
Mkulu wa bungweli, Sheikh Francis Iron, ayankhula izi pamapeto pa mpikisano owerenga bukhu m’mwezi wa Ramadhan lotchedwa ‘Chikhulupiliro cha Msilamu’ ndipo pamapeto pake opikisanawo anawafunsa mafunso.
“Izi zithandiza kuti akhale olimbika kuwerenga kuti adziwe za chipembezo chawo komanso ziwawonjezera chidwi choti adzikalimbikira kuwerenga ku Sukulu,” anatero a Iron.
Amene wapambana walandira K80,000 komanso bukhu la Quran, pamene opambana enawo alandira K50,000 ndi K30,000.
Olemba: Hassan Phiri