Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Tigwilizane ngati fuko limodzi

Nduna yoona zamaboma ang’ono umodzi ndichikhalidwe a Richard Chimwendo Banda apempha anthu kuti akhale ogwirizana kuti ntchito zachitukuko zipitilire kupita chitsogolo mdziko muno.

Iwo ayakhula izi pamwambo wachaka chino wachikhalidwe cha Atonga otchedwa ‘Mdauku wa Atonga’ ku Msani m’boma la Nkhata Bay komwe anayimilira mtsogoleri wadziko lino.

Asanayambe kuyankhula pamwambowo a Chimwendo Banda anayitana gule wa honala limodzi ndi aliyense yemwe anavala bwino ngati Ntonga kuti alowe mkati ndikuvina limodzi.

A Chimwendo Banda analangizanso mafumu kuti alewe mchitidwe wachinyengo panthawi yomwe akulemba anthu oti apindule ndi ndondomeko zaboma monga Mtukula Pakhomo.

Wapampando wa bungwe la Mdauku wa Atonga….., anati bungwe lawo ligwira ntchito limodzi ndi boma pa ntchito yobwezeretsa chilengedwe mchimake .

Iwo anatinso pali ganizo lomanga museum komanso sukulu pamalo omwe bungweli linagula ku Msani.

Pakali pano mtsogoleri wadziko lino wapereka ndalama zokwana K5 million kuti zithandizire ntchito zina ndi zina za bungwe la Mdauku wa Atonga.

 

Related posts

Boma lakhudzika ndi ngozi ya ku Kasungu

Romeo Umali

Ndondomeko ya mphamvu ku anthu yachiwiri akuikhazikitsa ku Lilongwe

Rabson Kondowe

‘Ntchito ya maphunziro ndi umoyo wabwino m’sukulu ikonzedwenso’

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.