Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering, The Jesus Nation, Mneneri Shepherd Bushiri wapempha andale ndi amipingo kuti ayambe ayiwala zakusiyana kwawo pandale ndi zikhulupiliro ndikuyamba kuthandiza a Malawi omwe akhudzidwa ndi njala maaka mmadera omwe kunagwa ngozi zogwa mwadzidzi.
A Bushiri alankhula izi kwa Mkando m’boma la Mulanje pomwe akupitiliza ntchito yogawa chimanga cha ulere kwa a Malawi ovutika ndi njala
Iwo ati ino sinthawi yolimbana pa ndale kapena zikhulupiliro koma yogwirana manja populumutsa miyoyo ya a Malawi omwe akusowa chakudya mmadera osiyanasiyana
“Chakudyachi ndikugawa kulikonse posaona kuti awa amatsatira chipani chanji kapena amapemphera mpingo uti, onse ovutika ndi njalawa ndi a Malawi,” atero a Bushiri.
Ntchitoyi tsopano yapindulira anthu am’maboma a Thyolo, Mulanje, Ntcheu komanso Lilongwe. Malinga ndi a Bushiri anthu pafupi-fupi 50,000 ndi omwe alandira thandizoli.
Pali chiyembekezo choti maboma enanso mdziko muno alandira thandizoli masiku akudzawa.
#mbconlineservices