Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Sitilora kuti atichitse manyazi pakhomo — Mpinganjira

A Bob Mpinganjira, amene ndi mphunzitsi wa timu yampira wa miyendo yadziko lino koma ya achisodzera, wati iwo salola kuti timuyi ichititse anthu manyazi pamene ikhale ikuchita nawo mpikisano wa mayiko anayi omwe ukhale ukuchitika kuyambira lero masana pa bwalo lamasewero la Bingu mumzinda wa Lilongwe.

Lero ndi tsiku lotsegulira masewero kwa achisodzera ndipo ntchito iyamba pamene timu ya Malawi ithambitsane ndi timu ya Zimbabwe.

A Mpinganjira ati awuza anyamata awo kuti asakhale ndi phuma ngati akufuna kuti apambane.

Lachisanu, timu ya Kenya idzasewera ndi Zimbabwe ndipo lamulungu, Malawi idzakumana ndi Kenya amene adzakhale masewero otsiriza.

Malinga ndi malamulo a mpikisanowu, yemwe adzapeze mapointi ochuluka ndi amene adzapambane.

Poyambilira, mu gawo la achisodzera, kumayenereka kukhala mpikisano wa kaphelachoka koma udasintha kaamba kakuti timu ya Zambia ya achisodzera inanena kuti siyichita nawo mpikisanowu pazifukwa zina.

Related posts

LET’S NOT SQUANDER THIS OPPORTUNITY- USI TELLS UN CLIMATE CONFERENCE

MBC Online

LCC demolishes illegal structures at Area 25

Romeo Umali

Lilongwe City Council demolishes Wadi Associates structures in Lilongwe

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.