Mkulu wabungwe lotolera misonkho, a John Biziwick, walamula kuti ogwira ntchito kubungweli aleke kugwiritsa ntchito msonkho okwera pa mabelo a zovala, umene anaukhazikitsa posachedwapa.
Izi zikudza patangodutsa nthawi yochepa ochita malonda amtunduwu munzinda wa Lilongwe atachita zionetsero ndikukapereka madandaulo awo ku ofesi za bungweli.