Apolisi ku Soche mumzinda wa Blantyre amanga Wonderful Itikani wazaka 41 pomuganizira kuti wapereka mimba kwa mwana wobereka yekha wazaka 14, yemwe wakhala akumugwililira kuchokera pomwe anali ndi zaka 10.
Mneneri wapolisi ku Soche, Aaron Chilala, wati Itikani ali ndi ana atatu ndipo uyu amene amagona nayeyu ndi wachiwiri kubadwa.
Malinga ndi a Chilala, woganiziridwayu amadzuka usiku ndikukalowa kuchipinda kwa mwanayo komwe amagona naye.
Ndipo dzana, mwanayo anadandaula kuti akumva kupweteka mmimba, zimene zinachititsa mayi ake kupita naye kuchipatala cha Queens kumene anawauza kuti ndiwoyembekezera.
Atamufunsa, mwanayo anaulura kuti bambo akewo akhala akumugwililira kuchokera chaka cha 2019.