Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani Sports

Pasuwa akukhulupilira kuti Bullets iyambaso kuchita bwino

Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Kalisto Pasuwa wati ali ndichikhulupiliro kuti timu yake iyambaso kuchita bwino mu Super League masana ano pamene akukumana ndi timu FOMO pabwalo la Kamuzu.

Bullets, yomwe ikuteteza ukatswiriwu, yasewera masewero 12 ndipo yapambana masewero atatu, kufanana mphamvu kasanu ndi katatu komanso kugonja kamodzi.

Timuyi ili panambala 6 ndi 17 points pamene FOMO ili panambala 12 ndi 14 points.

Masewerowa aonetsedwa pakanema wa MBC.

Mumasewero ena amene achitike masanawa, Creck Sporting Club ikumana ndi  Civil Service United pabwalo la Civo pamene MAFCO isewera ndi  Karonga United pabwalo la Chitowe.

Olemba: Praise Majawa

Related posts

CADECOM ithandiza mabanja omwe akhudzidwa ndi njala ku Phalombe

Romeo Umali

SWAM to host World Sports Day

Romeo Umali

Atsiriza kufufuza za imfa ya anthu asanu ku Blantyre

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.