Bungwe la Super League of Malawi (SULOM) mogwirizana ndi kampani ya TNM ati kuyambira pa 1 mwezi wa mawa anthu sadzawalola kulipira ndalama pamanja m`ma bwalo onse pamene tsopano adziguliratu matikiti a masewerowa a TNM Super League kudzera pa khadi ya Mpamba.
Izi zadziwika Lolemba ku Lilongwe pamene mbali ziwirizi zimafotokoza za momwe gawo loyeselera ndondomekoyi layendera kuyambira mwezi wa April chaka chino.
Mkulu oyendetsa ntchitoyi ku TNM, a Prince Sukasuka, ati iwo ndi okonzeka kuyamba kugwiritsa ntchito njirayi pamene akonza zonse zimene zimafunika kuti anthu adzitha kulipilira kudzera ku khadiyo.
Wapampando wa nthambi ya zamalonda ku bungwe la SULOM, a Chimwemwe Nyirenda, ati ndondomekoyi ithandiza kuchepetsa mchitidwe wakuba ndalama m’zipata, zomwe ati zipindulire kwambiri matimu a mu ligiyi.
Chaka chino, ndalama zimene zakhala zikupezeka ku masewero omwe anagwiritsa ntchito ndondomekoyi zakhala zikuchuluka kuposa ndondomeko yolipilira pa gate tsiku la masewero.