Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Nkhanza za m’banja zachuluka m’boma la Balaka – Apolisi

Apolisi m’boma la Balaka  adandaula ndi kukwera kwa chiwerengero cha milandu yokhuza nkhanza m’mawanja m’bomalo. 

Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, a Gladson M’bumpha, kuchokera mwezi wa January kufika mwezi wa June chaka chino m’bomalo alandira milandu yoposa 280  poyerekeza ndi milandu 180 mu nthawi ngati yomweyi chaka chatha.

Pakadali pano mlembi wamkulu wa bungwe lachipemebezo la Malawi Council of Churches (MCC), m’busa Alemekezeke Phiri wati mipingo mdziko muno ili ndikuthekera kothandiza kuchepetsa nkhanza m’banja.

Mwa zina m’busa Phiri wati  nchifukwa chake bungwe la MCC lakhala likuchititsa maphunziro m’maboma ena m’dziko muno kuphatikizapo la Balaka komwe akuphunzitsa atsogoleri a mipingo kuti mu ulaliki wawo adzikambamonso nkhani zokhudza kuipa kwa nkhanza mmabanja.

 

Olemba: Alufeyo Liyaya

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

There was overuse of antibiotics during COVID — WHO report

MBC Online

Joyous Celebrations concert preparations at 70%

Paul Mlowoka

We got you covered — NEEF

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.