Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

NEEF yakhazikitsa ngongole ya ulimi wa mthilira

Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lakhazikitsa ntchito ya ngongole yaza ulimi wa mthilira m’chigawo cha m’mphepete mwa nyanja.

Mkulu wabungweli, a Humphrey Mdyetseni, ati cholinga cha ntchitoyi ndi kufuna kuthana ndi vuto la njala m’dziko muno.

A Mdyetseni ati ndi khumbo la mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, kuti mitengo ya chimanga ikhale yokhazikika ndipo ndi chifukwa chake akulimbikitsa ulimi wa mthilira.

Iwo ati anthu akhala akulandira ngongolezi kufikira nyengo ya ulimi wodalira mvula itafikanso.

Mkulu waza ulimi m’boma la Salima, a Eniford Kanyimbo, wapempha alimi omwe apeze zipangizo za ulimizi kuti akumbukire kubweza ngongole akakolola zinthu zawo m’mwezi wa August chaka chino.

Kudzera ku ntchitoyi, anthu omwe apindule ndi oposa 200,000 ndipo adziwapatsa mbewu, fetereza komanso makina othililira oyendera mphamvu ya dzuwa.

Chaka chatha, bungwe la NEEF lidapereka ngongole yokwana K10.2 billion yothandizira ulimi wa mthilira ndipo anthu oposa 5,000 ndi omwe adapindula.

Related posts

DPP SETTLES FOR NAVICHA AS LEADER OF OPPOSITION

MBC Online

Likangala Irrigation Scheme projects K2.5 billion revenue from this year’s farming season

Alinafe Mlamba

Anthu ena akuonera nawo mwambo panja pa nyumba ya malamulo

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.