Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mukatengera chipani njala ikusautsani, watero Kalitendere

Phungu wanyumba ya malamulo wa dera la kumpoto chakummawa kwa boma la Machinga, Ajilu Kalitendere, walangiza anthu a m’dera lake kuti alandire ufa umene boma likugawa kutsatira njala imene yagwa m’dziko muno.

A Kalitendere amayankhula ku Nainunje kwa mfumu yaikulu Kapoloma ku Machinga kumene bungwe loona za ngozi zogwa mwadzidzidzi la DoDMA lagawa matumba a ufa okwana 1,254 kwa omwe akhudzidwa ndi njala.

Iye anauza anthuwo kuti akatengera zakuti MCP ndiyomwe ikugawa ufawo pomwe iwo ndi achipani china, afa ndi njala.

Wolemba: Davie Umar

Related posts

CHIKHO CHA CHAMPION KABVINA CHAFIKA PA K20 MILIYONI

MBC Online

Palibe mtsikana abwezedwe ku MUST chifukwa cha fizi — Prof. Malata

Alinafe Mlamba

MAREP 9 yathandiza anthu aku Dedza

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.