Mwamuna wazaka 42, Isaac Patisi, wakadzipereka ku polisi ya Area 3 ku Lilongwe atapha mkazi wake Azefa Kasamanda wazaka 36 pomukhapa ndi nkhwangwa.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati izi zachitika ku dera la Malingunde m’boma lomwelo la Lilongwe.
Malinga ndi a Chigalu, mwamunayu anakangana ndi mkazi wake usiku pomuganizira kuti ali pa ubwenzi wamseli ndi mwamuna wina.
Mkangangano utakula, Patisi anadzuka ndikutenga nkhwangwa kukhapa mkazi wakeyo pachifuwa iye ndikuthawa.
Kenako mwamunayo anafotokozera mchemwali wa malemuyo zankhaniyi asanakadzipereke kupolisi.