AChewa pansi pa bungwe lawo la Chewa Heritage Foundation (CHEFO) atsekulira mudzi wa aChewa, m’mudzi wa Msampha, mfumu yaikulu Chadza m’boma la Lilongwe.
Mudzi wa aChewa ndi malo omwe aChewa, pansi pa bungwe lawo, anagula kuti adzichitirapo zochitika zosiyanasiyana kuphatikiza mwambo wokondwelera chikhalidwe chawo.
Pamwambowu pafika mafumu, anthu ochokera mmadera osiyanasiyana komanso Gule wa mkulu ochokera m’maboma omwe kumapezeka aChewa.
Mlendo olemekezeka pamwambowu ndi a Napoleon Dzombe, mmodzi wa akuluakulu odziwika bwino pa ntchito za malonda mdziko muno.
Wa pampando wa CHEFO, a Stanley Chakhumbira Khaila ati pamalowa adzakhazikitsapo, malo okopa alendo, Tourism Cultural Centre, yomwe idzakhale ndi Nyumba yosungirako mabukhu (Library), Museum komanso malo odyera, mwa zina.
Mwambowu ukuchitika pa nthawi yomwe aChewa akukonzekera mwambo wa Kulamba omwe uchitike ku Nkaika, mdziko la Zambia, komwe amapereka ulemu kwa Kalonga Gawa Undi, mfumu yaikulu ya aChewa mmaiko a Malawi, Zambia komanso Mozambique.
Olemba Yamikani Simutowe