Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Abusa asiye kudalira nkhosa zawo pachuma

Kampani ya Synthesis Agriculture yalangiza  abusa ena kuti asiye kudalira nkhosa zawo pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndipo m’malo mwake ayambe kugwira ntchito zaulimi kuti azidzithandiza okha.

M’modzi mwa akuluakulu ku kampaniyi a Aaron Chitimbe wati nthawi yakwana  yoti abusa ayambe kudzidalira  pachuma.

Iwo ati pamene abusa akuwuza anthu kuti adzapita kumwamba akuyenera kudziwanso kuti asananyamuke ulendo wakumwamba akuyenera kuti akhale ndi chakudya padziko lapansi  pompano.

A Chitimbe alankhula izi pamaphunziro omwe cholinga chake ndikulimbikitsa abusa ubwino wochita ulimi pamene akukonzekera kupuma pantchito omwe akuchitikira mu mzinda wa Blantyre.

Maphunzirowa abweretsa pamodzi atumiki a Mulungu ochokera m’maboma osiyanasiyana chigawo cha kum’mwera.

Related posts

Mw geared to end Cholera by 2030

Romeo Umali

We will make the country proud — Fazili

Romeo Umali

Chakwera advises acting Justices to keep composed temperament

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.