Bwalo la Milandu la High Court mumzinda wa Lilongwe lathetseratu mlandu wa pakati pa ochita malonda a ku Nsungwi, Area 25 ndi m’mwenye Akbar Salahudding popeza umboni okwanira palibepo.
A Akbar anakasumira anthu ochita malondawa potsatira lamulo lochokera ku unduna wa za malonda loti atseke shopu yawo pa 8 April chaka chino ati kaamba kakuti amawaganizira kuti ‘amatsitsa kwambiri mitengo ndi kuphangira pochita malonda’.
Oyimila mlandu anthuwa, a Wesley Namasala, ati iwo tsopano akufuna ndalama ya chipepeso chifukwa akhala akuononga ndalama zambiri popita ku bwaloli.
A Namasala aopseza kuti bwalo la milandu lidzaunikira za mlingo wa ndalama zomwe iwo akufuna ngati samvanapo.
Justice Kenyatta Nyirenda ndi amene amaunika mlanduwu ndipo sabata yathayi mlanduwu adawuyimitsa pofuna kuti mbali zonse ziwiri ndi owaimira pa milandu aunikire bwino kalata zofunika pa nkhaniyi.
#MBCDigital
#Manthu