Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Sports Sports

Bullets yapanga ubale ndi Sun Group

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yasainilana m’gwirizano ndi kampani ya Sun Group imene idzipereka madzi akumwa.

Izi zikubwera pamene mkulu oyendetsa ntchito ku Bullets a Albert Chigoga ati timu yawo imaononga ndalama zosachepera K 20 million pogula madzi akumwa.

Sameer Ahmad, mkulu wa kampani ya Sun Group, wati iwo asankha kuthandiza timuyi kaamba kakuti imachita zinthu zake mwa dongosolo komanso ili ndi kuthekera kopititsa ntchito za kampaniyi pamwamba.

Sun Group imadziwika bwino popanga zinthu zosiyanasiyana monga mafuta ophikira, ufa komanso soya pieces.

Bullets ikhala ndi masewero ake oyamba mu ligi yayikulu ya chaka chino pomwe ikumane ndi Dedza Dynamos pa bwalo la Dedza loweruka.

#MBCDigital
#Manthu

Related posts

Alimi asamale pogula mbewu — Self Help Africa

Romeo Umali

MBC rolls out Ngwe Ngwe Ngwe project open days

Rabson Kondowe

COMFWB calls for collaborative efforts among women entrepreneurs

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.