Malawi Broadcasting Corporation
Local Local Nkhani

MEC yalengeza zotsatira za chisankho cha komiti yayikulu ya DPP

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) yalengeza zotsatira za chisankho cha komiti yaikulu ya chipani cha Democratic Progressive.

A Joseph Mwanamvekha agonjetsa a George Chaponda ndi kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi m’chigawo cha kum’mwera.

A Bright Msaka awasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa DPP mchigawo cha kum’mawa.

A Alfred Gangata apambana ndikukhala wachiwiri kwa prezidenti wa chipani cha DPP m’chigawo chapakati atapikisana ndi a Paul Gadama.

A Jappie Mhango alowa opanda opikisana naye kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP m’chigawo cha kumpoto.

Pa udindo wa mlembi wamkulu wa DPP, a Peter Mukhito agonjetsa a Clement Mwale.

Pa udindo wa mkulu okonza za zochitikachitika m’chipanichi (National Organising Secretary), a Sameer Suleman agonjetsa a Chimwemwe Chipungu.

Pa udindo wa  Director of operations a Charles Mchacha ndiwo apambana.

Ndipo mkulu owona zamalamulo mu chipanichi, a Chipiliro Mpinganjira agonjetsa a Charles Mhango.

A Mary Navicha ndiwo asankhidwa pa udindo wa mkulu owona za amayi.

A Gladys Ganda, asankhidwa pa udindo wa mkulu owona zachisankho.

Pa mpando wa mkulu owona za achinyamata, a Norman Chisale awasankha atagonjetsa anthu ena atatu.

A Ben Phiri asankhidwa kukhala mkulu owona za ndale mchipanichi (Director of Political Affairs.)

Pa udindo wa mkulu owona zachuma pali a Ralph Juma omwe agonjetsa a Malison Ndau.

Ndipo a Timothy Khoviwa alowa pa udindo woona zachipemvedzo ( Director of Religious Affairs) popanda opikisana nawo.

A Fyness Mwagonjwa awasankha kukhala paudindo wazosamalira anthu (Director of Social Services) atagonjetsa amai ena atatu.

Awa ndi maudindo akuluakulu ndipo palinso ma udindo ena omwe a MEC alengeza kale.

Related posts

Polisi yadandaula ndi zilango zofewa pa milandu yoononga chilengedwe

Romeo Umali

UNDP offers advice to foster SME growth in Malawi

Romeo Umali

Mwambo wa Kulamba ulipo chaka chino

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.