Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Mbava ipempha chilango chofewa chifukwa anayigulula mano

Mbava zitatu ku Phalombe zinapempha khothi kuti liwapatse chilango chofewa kaamba koti tsiku lomwe zinagwidwa  anthu mderalo anazimenya kwambiri mpaka imodzi mwa mbavazo anayigulula mano awiri.

Mneneri wapolisi ku Phalombe, Jimmy Kapanja, wati atatuwo ndi  Nyadani Mandevu wazaka 39, wa m’boma la Zomba, Kingsley Mulotiwa wazaka 22 ndi Eric Muwawa wazaka 26, awiriwa ochokera kwa Namasoko ku Phalombe.

Malinga ndi a Kapanja, mbavazo, zomwe  zinali ndi zida zowopsa kuphatikizapo zikwanje, zinathyola nyumba ziwiri m’bomalo ndikuba njinga zamoto ziwiri ndi ndalama pafupifupi K1 million ndikuthawa.

Patadutsa masiku angapo, apolisi anagwira mbavazo ndipo zitakaonekera kukhothi, zinapempha chilango chofewa koma woweruza milandu sanamvere izi moti zikakhala ku ndende zaka 8 aliyense.

Related posts

Treasury lauds Standard Bank for innovative, customer centred principles

Romeo Umali

Govt. pledges stronger action to restore degraded environment

Beatrice Mwape

Malawian Artists set to shine at Jamaica’s Reggae Month

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.