Unduna wa zamasewero wati ndi okondwa ndi luso limene laoneka pa mpikisano opalasa njinga ku Lilongwe, pamene bungwe la African Union Sports Council of Region 5 likukondwelera kuti lakwanitsa zaka 25.
Mlembi mu undunawu, a Chikumbutso Mtumodzi, anati boma liyesetsa kuthandiza masewerowa kudzera ku bungwe lowayendetsa la Cycling Federation of Malawi.
A Mtumodzi anati izi zili chomwechi chifukwa awona kuti masewerowa ali ndi tsogolo lowala ngati patakhala chidwi cha chikulu chowatukula kuchokera ku makampani komanso anthu osiyanasiyana akufuna kwabwino.
Pampikisanowu, a Peter Zulu ndi amene apambana atapalasa njinga pa mtunda wa makilomita 100 ndipo walandira mphotho yaikulu ya K600, 000.
A Rashid Aufi wakhala kwatswiri pa mtunda wa makilomita 50 ndipo walandira K300, 000.
Olemba: Batuel Gerald