Ofesi yoyang’anira za chisamaliro cha anthu m’boma la Likoma yati kusowa kwa chidwi cha makolo pa ana awo ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe zikukolezera kuti mimba za ana achichepere zikwere.
Ofesiyi imayankhapo pa zakafukufuku yemwe anatulutsa mu unduna wa za umoyo m’mwezi wa July chaka chino, yemwe anaonetsa kuti bomali lili pachiwiri pa mndandanda wa kumene kuli chiwelengero chokwera kwambiri cha mimba za ana.
Ogwirizira udindo wa wamkulu mu ofesiyi, a Felix Banda, wati kaamba ka usodzi, makolo amayika chidwi chawo chambiri kunyanja, zimene zimawapatsa ana mpata ochuluka opanga zinthu opanda owaletsa.
Komabe, a Banda anaonjezera kuti zina mwazifukwa zomwe zikukweza chiwerengerochi ndi kaamba kakuti anthu a m’dziko la Mozambique akabwera kudzachilira pa chilumbachi, chiwerengero chonse chimatengedwa ngati ndi cha anthu aku Likoma.
Iwo anatinso kusowa kwa mabungwe othana ndi mchitidwewu kwakhudza kwambiri chilumbachi chifukwa, padakali pano, ndi boma lokha lomwe likugwira ntchitoyi.
Ngakhale zili chomwechi, a Banda anati ofesi yawo mothandizana ndi apolisi komanso mafumu akhazikitsa makomiti amadera omwe adzidzathandiza kuneneza zamchitidwe oterowo m’madera mwawo ndipo anatsindika kuti pali chikhulupiliro kuti zinthu zisintha.
Olemba: Vicky Mphande, Likoma

