Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kapusa aikidwa m’manda

Mwambo oika mmanda malemu Geofrey Kapusa uli mkati mmudzi mwa Mkanda kwa Ngulumia ku Zomba, komwe ndi kumudzi kwawo.

Anthu osiyanasiyana, kuphatikizapo aphungu anyumba yamalamulo, mkulu wa Malawi Broacasting Corporation a George Kasakula ndi ena ochuluka ali nawo pamwambowu.

Mwana wake oyamba wa Geofrey, Elizabeth, anati ndi okondwa kuti bambo ake amwalira ali okondwa chifukwa anali atapereka moyo wawo m’manja mwa chauta.

Iye wathokoza anthu osiyanasiyana monga nduna ya zamadzi, mayi Abida Mia komanso MBC chifukwa chothandiza bambo ake kuyambira ali ku chipatala kufikira pamene akuyikidwa m’manda.

Related posts

‘Andale ena akumatenga anthu ammadera akutali kudzawalembetsa mkaundula wa voti’

Rabson Kondowe

OVER 200, 000 JABBED AGAINST COVID -19 IN MANGOCHI

MBC Online

Bullets vs Eagles at BNS

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.