Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Osewera akale a Flames aimba lokoma

Wapampando wa kampani ya Ekhaya Farm’s Foods, Thom Mpinganjira wapereka K17 million kwa osewera mpira akale omwe anachita zakupsa mzaka za 1978 ndi 1979 komanso 1988 pomwe timu yadziko lino inaatenga zikho za East and Central African Challenge Cup.

Mpinganjira wati ndalamayo wapereka ndicholinga chofuna kulimbikitsa osewera achisodzera zakufunikira kotumikira dziko modzipereka ngati momwe ankachitira akuluakuluwa.

Iye wayamikiranso mkulu wa JK productions, a Jim Kalua, kaamba koyambitsa bungwe lothandiza akatswiri akalewa.

Ndipo nduna ya zamasewelo, a Uchizi Mkandawire, ati zomwe achita a Ekhaya ndichitsimikizo kuti m’dziko muno muli anthu omwe amakonda mpira.

Ena mwa akuluakulu omwe anali nawo pamwambowu ndi mtsogoleri wa bungwe loyendetsa mpira wamiyendo m’dziko mdziko muno, a Fleetwood Haiya, mtsogoleri wa bungwe la Super league of Malawi, Gilbert Mitawa komanso mfumu yaikulu ya mzinda wa Lilongwe, Richard Banda.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mwala otayidwa unasanduka mwala wapangodya, watero Msonda

MBC Online

Ripple Africa disposes illegal fishing gear in KK

Beatrice Mwape

Centenary Bank partners with Tourism Ministry

Yamikani Simutowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.